Kodi nkhani ya Exchange Rate ndi Devaluation imayenda bwanji?
Ukakhala ndi $1, Ku Bank akakupatsa K1,733.40 koma pa Black Market akakupatsa K4,500. Zikuwoneka kupindula kusintha ndalama pa Black Market, sichoncho?
So akamanena kuti mphamvu ya Kwacha ku Bank ifanane ndi ya ku Bank amathanthauza kuti:
Ukakhala ndi $1, ku Bank adzikupatsa K4,500 chimodzi-modzi ndi Black Market. Vuto ndilakuti ukafuna kupeze $1, ku Bank ukayenera kuperekanso K4,500 chimodzi-modzi pa Black Market.
Ku Malawi, vuto logwetsa ndalama kuchoka pa $1 = K1,733.40 kufika pa $1=K4,500 ndilakuti kuno ku Malawi timadalira katundu wochokera kunja monga fertilizer, mankhwala, mafuta a galimoto, kungonenapo zochepa.
Tiyerekeze kuti kunja fertilizer wa 50Kg ali pa $100. Pamene tili pa $1=K1,733.40, mtengo wa fertilizer tikugula pa K173,340.00. Koma tikagwetsa Kwacha kuti ikwale $1=K4,500 fertlizer tidzigula K450,000. Kodi pali phindu lanji? Tifere dyera lopeza $1 pa mtengo wosavomerezeka pamene tikufa chifukwa cha fertelizer, mankhwala, mafuta ndi zina?
Tikamasintha $1 pa mtengo wovomerezeka ku Bank, timathandiza kuti ndalama zogula fertilizer zizipezeka ku Bank. Koma tikamasintha $1 pa Black Market pa mtengo wosavomerezeka, timathandiza kuti ndalama zogulira fertilizer zisapezeke ku Bank.
Ndibwino kusintha $1 ku Bank pa mtengo wovomerezeka ngakhale ili yochepa tikudziwa kuti tikuthandiza ndalama yogulira fertilizer, mankhwala, mafuta yizipezeka ku Bank kuposa kusintha pa Black Market chifukwa cha dyera kuteroku tikuthandiza kuti ndalama ya fertilizer, mankhwala, mafuta isamapezeke ku Bank.
Dyera ndiloyipa lidzatiphetsa.

No comments:
Post a Comment